27/07/2026
M'MENE MUNGASANKHIRE SOLAR SYSTEM YOYENERA PANYUMBA PANU
Anthu ambiri amagula solar system chifukwa yatchipa. Koma yotsika mtengo si nthawi zonse imakhala yabwino, ndipo ingakuwonongereni ndalama zambiri mtsogolo.
Musanagule, dzifunseni mafunso 5 awa:
✅ 1. Mukufuna kuyatsa kapena kugwiritsa ntchito zipangizo ziti?
Ganizirani zipangizo zomwe mukufuna kugwiritsa ntchito, monga mababu, TV, firiji, mafani kapena ku charger mafoni. Kuchuluka kwa zipangizo kumathandiza kudziwa kukula kwa solar system yomwe mukufuna.
✅ 2. Mukufuna magetsi azikhala kwa maola angati?
Ngati mukufuna kuunikira usiku wokha, solar system yaying'ono ndiyokwanira. Koma ngati mukufuna usana ndi usiku kapena nthawi yayitali pomwe magetsi a ESCOM azima, mudzafunika batire lokhala ndi mphamvu zambiri.
✅ 3. Kodi batire ndi labwino komanso yolimba?
Batire ndi mtima wa solar system. Mabatire a Lithium nthawi zambiri amakhala nthawi yaitali, safuna kukonzedwa pafupipafu poyerekeza ndi mabatire ena.
✅ 4. Kodi ma solar panel angathe kupanga mphamvu zokwanira?
Ma solar panel ayenera kukhala ogwirizana ndi kukula kwa batire komanso kuchuluka kwa mphamvu zomwe mumafunikira tsiku ndi tsiku. Ngati panel ndi yaying'ono kwambiri, batire silidzadza mokwanira.
✅ 5. Kodi pali chitsimikizo (Warranty) ndi thandizo pambuyo pogula?
Nthawi zonse gulani kwa kampani yomwe imapereka chitsimikizo cha malonda, ntchito yoyika (installation), komanso thandizo mukakumana ndi vuto.
💡 Kumbukirani: Solar system yabwino si yotsika mtengo kwambiri, koma ndi yomwe imakwaniritsa zosowa zanu za magetsi tsiku lililonse, modalirika komanso kwa nthawi yaitali.
Mukafuna kudziwa solar system yoyenera nyumba kapena bizinesi yanu,
📲 Titumizireni uthenga pa WhatsApp lero ku 0988910785 kuti tikupatseni upangiri WAULERE wokuthandizani kusankha solar system yoyenera bajeti ndi zosowa zanu. Kapena pangani follow page yathu kuti mudziwe zambiri.