Hon. Esther Majaza MP - Mchinji North East Constituency

Hon. Esther Majaza MP -  Mchinji North East Constituency Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Hon. Esther Majaza MP - Mchinji North East Constituency, P/Bag 1 kapiri , Mchinji, Lilongwe.

Hello, Hello Azibale anga okondedwa kuno kwathu Ku Kapiri, Kkkkk tasowanatu kkkkk 😃😃😃 Ndilipo ine Mlongo wanu , mwana wa...
10/05/2025

Hello, Hello Azibale anga okondedwa kuno kwathu Ku Kapiri,

Kkkkk tasowanatu kkkkk 😃😃😃 Ndilipo ine Mlongo wanu , mwana wanu ndipo zazikulu zikuchitika ndipo zichitika ndithu osadandaula, osaopa koma chinthu chimodzi tisunge umodzi paja Nkhondo simanga mudzi ndie zambiri zizikambidwa koma osabweza mau oipa kwaoipawo pewani ndithu azibale anga.

Komano lero ndine munthu osangalala kwambiri kuona ndikuva kuti nkhani imene anzathu ochita malonda pa Msika wathu yatha kubwalo la Milandu Ku Lilongwe ndipo pali chiyembekezo kuti tsopano maloto athu ikhala ndi Msika wamakono aphelezera. Ndipo ndithokoze anzathu ochita malondawa potengela nkhani Ku bwalo lamilandu kuti apeze thandizo la chilungamo pa Malo amene Iwo amachitilapo malonda ndipo izi zasonyeza kuti ngakhale chitukuko chili chofunika komabe tisamafele mmazila pofunafuna chilungamo chammene ndondomeko ya chitukuko chiliri.

Ndiloreni ndithokoze Gogo Senior Chief Dambe chifukwa chosatopa kulondoloza nkhani imeneyi kuti chilungamo chioneke ndipo Agogo ndi Mafumu Anu onse osaiwala a Group Village Nthema mumve kukuyamikilani simunatope pofunitsitsa kuti chilungamo chioneke chimene chinatchinga chitukuko chofunikilachi mdela lathu. Ambuye akudalutseni kopambana.

Achinyamata ndi mzika zonse kuno Ku Kapiri nanuso munayesetsa kutilimbikitsa kutiwunikila komaso kuyenda nafe posayang'ana zipsyinjo zimene zinalipo tiyeni tipitilize kupanga zinthu zotele zimene ndizothandiza kutukula Dela lathu. Ine ngati Phungu wanu ndine osangalala koposa. Ndipo Ambuye akudalutseni kopambana.

21/04/2025
Mau pang' ono zitukuko mbweeeeNdale pambuyo Chitukuko patsogolo Mau - Mau ground kusintha maonekedwe akale ndikuwoneka m...
19/04/2025

Mau pang' ono zitukuko mbweeee
Ndale pambuyo Chitukuko patsogolo
Mau - Mau ground kusintha maonekedwe akale ndikuwoneka mwatsopano.
Lero tikuika zotchinga zambali za mawaya. Chitukuko ichi ndi cha dera lathu ndipo ndi Cha wina aliyense.
. Chakwera chongu
👏 Majaza Chonguuu
. Chikoti Councilor Chonguuu
🐓🐓🐓🐓🐓🐓🐓🐓🐓🐓🐓🐓🐓

19/04/2025

Big shout out to my newest top fans! Vincent Manyasi, Luka Mikili, Timothy Basikolo, Innocent Phiri, Mphatso Gowelo, Emey Kanyenda Kazako, Rodwell K S Roksy, Mussah James Monjeza, Kondwani Tiwo Maseko, Chilungamo Kuwawa, Wilson Mbeta Banda, Beston Willie Chingaru

Ground lomwe limatchuka ndi dzina lakuti Mau - Mau  ground lero lasintha maonekedwe ake pomwe ine monga  Phungu wanu wac...
19/04/2025

Ground lomwe limatchuka ndi dzina lakuti Mau - Mau ground lero lasintha maonekedwe ake pomwe ine monga Phungu wanu wachizimai wa dera lino ndikumalizitsa Stadium yomwe tidayamba kumanga mbuyomu. Lero tikuika mawaya otchinga mbali kuzunguliza ground lonse. Awa ndi masophenya a Dr. Chakwera kuti Achinyamata azikhala ndi ma ground abwino ochitira masewero abwino.
. Chakwera chongu
. Majaza MP chonguuu
. Chikoti Councilor Chonguuu
SITIKUSINTHA 🔥🔥🔥

12/04/2025

mugone bwino anthu anga nonse !!!

Layenda bwanji tsiku la lero azibale anga nonse. Ife ndale tipangabe kutsogoloku ndamva kuti anthu akuyenda ndi usiku om...
12/04/2025

Layenda bwanji tsiku la lero azibale anga nonse. Ife ndale tipangabe kutsogoloku ndamva kuti anthu akuyenda ndi usiku omwe ngati fisi kunyengelera anthu amene amanama kuti anawasankha kale aja angodikila kulumbilitsidwa kkkkkk koma abale ndale zitizuza mpaka kumayenda ndusiku mukuopa chani masana 🤣🤣🤣🤣

Henewe 😃😃😃 ine ndimati ndikudziwitseni kuti Stadium ija ikutheka ndithu weziwezi lero waya wafika ndipo week iyiyo akhala ataikidwa ndithu. Ndipo ndikukutsimikizilani kuti Stadium yathu tiimaliza.

Awowo akamalongolora osadabwa amene amadziwa zisisi za gule ndamene anapitako za CDF timazidziwa ndife mmene imayendela ndipo ndifeyo tinawapempha apule kuti ikwele ncholinga choti tizipangako zolozeka popeza ndiyogawidwa mmagawo ndipo imapelekedwaso magawo simabwela pakamodzi ndie awowo awo ndikayamba ndale ndiwayedzeka osadandaula. 🤣🤣🤣🤣

Usiku wabwino kwaife tonse . Ambuye wazifundo zochuluka atiyang'anila tonse 🙏🙏



Hello, Hello. As am wishing His Excellency the State President Dr Lazarus Chakwera a Happy Birthday today. I have this p...
05/04/2025

Hello, Hello.

As am wishing His Excellency the State President Dr Lazarus Chakwera a Happy Birthday today. I have this proverb that Your Excellency and my fellow Mchinji North East Constituents can take, is this that "Kukuwa kwa agalu sikubweza Mkango komwe walinga" Therefore let's keep going and let's not lose focus pajatu Ambuye anatiphuzitsa za Anamwali khumi pomwe asanu mwaiwo chifukwa chakuti sadalowe nawo nkati mwanyumba ya mkwati anayima pa window nkumatukwana kupeputsa ukwati kuiwala kuti vuto linali lopeweka koma iwo sadafune kutelo chifukwa chikonda kudalira ena choncho momwemo ndi awowo.

Mwaswela bwanji azibale anga pamene tikukonzekela zisankho chaka chino ndikukupemphani kuti tichite ndale zathu mwabata ...
04/04/2025

Mwaswela bwanji azibale anga pamene tikukonzekela zisankho chaka chino ndikukupemphani kuti tichite ndale zathu mwabata ndi chikondi chifukwa tonse ndife mzika ndi ana a Senior Chief Dambe komaso Agogo TA Kapondo ndale zisatigawanitse.

Chinaso ndichakuti inu ndi ine tachita bwino ndithu muzaka zimene ine munandipatsa koyamba kuti ndikutumikileni Ku Nyumba ya Malamulo. Zitukuko zikuoneka ndithu kotelo tilibe chifukwa choopa amene Ali ndimaloto ofuna kubwezeleza Dela lino m'mbuyo. Choncho mtima pansi Dela lino ndilotetezeka ndipo pamodzi ndi Dr Laz Chitukuko patsogolo basi.

Sitilora kuti vote yathu wina akapezele Visa yopitila Ku America kuno atatiimitsila chitukuko.






Azibambo Atalephera kubweretsa Chipatala pa Kapiri pano lero nditha kukutsimikizirani kuti ine phungu wanu  wachizimai n...
18/03/2025

Azibambo Atalephera kubweretsa Chipatala pa Kapiri pano lero nditha kukutsimikizirani kuti ine phungu wanu wachizimai ndapanga Chitukukochi mudzi mwa CHIKOTI ndipo titsegulira posachedwapa.

Atalephera azibambo kumanga Police yabwino, Lero nditha kukutsimikizirani kuti tapitani pa Kapiri Police mukawone nokha zomwe ine Phungu wanu mdera lino ndachita. Kapiri New police idatha ndipo titsegulira soon.
. Chakwera chonguuu #
. Esther Majaza MP Chonguuu #
.Chikoti councilor Chonguuu #

Za ground, Madzi a Mipopi, Mijigo, Magetsi a Mphamvu ya solar muma school, magetsi a Mphamvu ya solar mu msika ndi ma Trading anthu, kuphunzitsa azimai 1,000 ntchito za manja monga baking, cooking, kupanga soap , kulipilira ana school fees, kuphunzitsa achinyamata ntchito zosiyana siyana zonse izi tizakambabe.

ESTHER MAJAZA MP Apweteka ma team kuti khaaaa khaaaa khaaaa

Address

P/Bag 1 Kapiri , Mchinji
Lilongwe

Telephone

+265996358820

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Hon. Esther Majaza MP - Mchinji North East Constituency posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to Hon. Esther Majaza MP - Mchinji North East Constituency:

Share