01/06/2026
WHEN YOU ARE IN ROME,DO WHAT THE ROMANS DO.
To translate this proverb in our native language I can say;.....
Ukaona azako akukazinga maso naweso kazinga akowo or ukakhala ku Roma uzipanga zomwe ma roman akuchita.
Mwambi uyu umandiphudzitsa kenakake kwambiri.
Kodi ma roman omwe akunenedwa umu mukuwadziwa Inu?Ma roman amene akunenedwa umu siinuyo ayi.
Ma roman amenewatu si Inu koma ndi Bushiri ndi mpinganjira.
Ma roman amenewa ndikuti siinu ndi Jimmy koreya Mpansa ndi Simbi Phiri.
Inu ma Romani amenewa ndi anthu olememela osati inuyo ayi simudafike pokhala aroma inuyo.
UKUTATHAUZA CHANI MWAMBI UMENEWU.
Ukutathauza kuti tidzikhala ndi chidwi kumaona olemela zomwe akupanga ndipo zomwe akupangazo tidziziona ndikumazitsatila ndichifukwa akuti when you are in Rome let's do what the roman do.
Mpinganjilati Inu sagula kapilipili amalima mugadeni yake.
Napoleon Zombe uja ine sagula mpiru amalima mugalideni yake.
Ndikuti Bushiri sangagule nkhwani ayi sapanga nawo izizi.
Pomwe iwe ndi sabola yemwe wakapilipili kuchita kukagula kutsika mwalo mongobzala pakhomo pako mpompo.Mpiru omweu, Chinese yemweyi,mwalo mongodzala panyumbapo Kuma saver ndalama koma chilichonse utulutse ndalama nthumba ndizoona mchimwene.akuti mudzipanga zomwe ma Romani akuchita kapena kuti mudzipanga achina Simbi, Bushiri,Mpinganjira akupanga mwambiutu ukutelo.
Anthu achumatu amaseva ndalama kwambiri.Omwe timaononga ndalama mwachisawawa ndiosaukefe.Tiyeni zinazi tidzidzipangila yokha plz osangoti ndi sabola yemwe kukagula ayi tiyeni tichepetse azanga.